5 Amenewo ndipo anagawa zisi za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa cinenedwe cao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.
6 Ndi ana amuna a Hamu: Kusi, ndi Mizraimu, ndi Puti, ndi Kanani.
7 Ndi ana amuna a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka; ndi ana a Raama: Sheba ndi Dedane.
8 Ndipo Kusi anabala Nimrode; ndipo iye anayamba kukhala wamphamvu pa dziko lapansi.
9 Iye ndiye mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova: cifukwa cace kunanenedwa, Monga Nimrode mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova.
10 Ndipo kuyamba kwace kwa ufumu wace kunali Babele, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara.
11 M'dziko momwemo iye anaturuka kunka ku Ashuri, namanga Nineve, ndi mudzi wa Rehoboti, ndi Kala,