12 Khutu lakumva, ndi diso lopenya,Yehova anapanga onse awiriwo.
13 Usakonde tulo ungasauke;Phenyula maso, udzakhuta zakudya.
14 Wogula ati, Cacabe cimeneco.Koma atacoka adzitama.
15 Alipo golidi ndi ngale zambiri;Koma milomo yodziwa ndiyo cokometsera ca mtengo wapatari.
16 Tenga maraya a woperekera mlendo cikole;Woperekera mkazi wacilendo cikole umgwire mwini.
17 Zakudya za cinyengo zikondweretsa munthu;Koma pambuyo pace m'kamwa mwace mudzadzala tinsangalabwi.
18 Uphungu utsimikiza zolingalira,Ponya nkhondo utapanga upo.