7 Wosunga cilamulo ndiye mwana wozindikira;Koma mnzao wa adyera acititsa atate wace manyazi.
8 Wocurukitsa cuma cace, pokongoletsa ndi phindu,Angokundikira yemwe acitira osauka cisoni.
9 Wopewetsa khutu lace kuti asamve cilamulo,Ngakhale pemphero lace linyansa.
10 Wosoceretsa oongoka mtima alowe m'njira yoipa,Adzagwa mwini m'dzenje lace;Koma angwiro adzalandira colowa cabwino.
11 Wolemera adziyesa wanzeru;Koma wosauka wozindikira aululitsa zace.
12 Posekera olungama pali ulemerero wambiri;Koma pouka oipa anthu amabisala.
13 Wobisa macimo ace sadzaona mwai;Koma wakuwabvomereza, nawasiya adzacitidwa cifundo.