1 Mwananga, ngati waperekera mnzako cikole,Ngati wapangana kulipirira mlendo,
2 Wakodwa ndi mau a m'kamwa mwako,Wagwidwa ndi mau a m'kamwa mwako.
3 Cita ici tsono; mwananga, nudzipulumutse;Popeza walowa m'dzanja la mnzako,Pita nudzicepetse, numdandaulire mnzako,
4 Usaone tulo m'maso mwako,Ngakhale kuodzera zikope zako.