10 Kodi pali kanthu unganene kuti, Taona katsopano aka? Kanalipo kale, kale lomwe tisanabadwe ife.
11 Zoyamba zija sizikumbukiridwa; ngakhale zomwe zirinkudzazo, omwe adzakhalabe m'tsogolomo, sadzazikumbukirai.
12 Ine Mlaliki ndinali mfumu ya: Israyeli m'Yerusalemu.
13 Ndipo ndinapereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimacitidwa pansi pa thambo; nchito yobvuta imeneyi Mulungu apatsa ana a anthu akasauke nayo.
14 Ndaona nchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi cabe ndi kungosautsa mtima.
15 Cokhotakhota sicingaongokenso; ndipo coperewera sicingawerengedwe.
16 Ndinalankhula ndi mtima wanga, ndi kuti, Taona, ndakuza ndi kudzienjezera nzeru koposa onse anakhala m'Yerusalemu ndisanabadwe ine; inde mtima wanga wapenyera kwambiri nzeru ndi cidziwitso.