10 Yehova waturutsa cilungamo cathu; tiyeni tilalikire m'Ziyoni nchito ya Yehova Mulungu wathu.
11 Nolani mibvi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; cifukwa alingalirira Babulo kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera cilango kwa Yehova; kubwezera cilango cifukwa ca Kacisi wace.
12 Muwakwezere mbendera makoma a Babulo, mulimbikitse ulonda, muike alonda, mupangiretu olalira, pakuti Yehova waganiziratu ndi kucita comwe ananena za okhala m'Babulo.
13 Iwe wokhala pa madzi ambiri, wocuruka cuma, cimariziro cako cafika, cilekezero ca kusirira kwako.
14 Yehova wa makamu walumbira pa Iye mwini, kuti, Ndithu ndidzakudzaza iwe ndi anthu, monga ndi madzombe; ndipo adzakukwezera iwe mpfuu.
15 Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yace, wakhazika dziko lapansi ndi nzeru yace, ndi luso anayala thambo;
16 pamene Iye anena mau, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, ayesa mphezi ya mvula, aturutsa mphepo ya m'nyumba za cuma zace.