12 Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale cakukuyesani, ngati cinthu cacilendo cacitika nanu:
13 koma popeza mulawana ndi Kristu zowawa zace, kondwerani; kutinso pa bvumbulutso la ulemerero wace mukakondwere kwakukurukuru.
14 Mukatonzedwa pa dzina la Kristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.
15 Pakuti asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wocita zoipa, kapena ngati wodudukira;
16 koma akamva zowawa ngati Mkristu asacite manyazi; koma alemekeze Mulungu m'dzina ili.
17 Cifukwa yafika nthawi kuti ciweruziro ciyambe pa nyumba ya Mulungu; komangati ciyamba ndi ife, citsiriziro ca iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu cidzakhala ciani?
18 Ndipo ngati munthu wolungama apulumuka ndi kuyesetsa kokha kokha, munthu wosapembedza ndi wocimwa adzaoneka kuti?