1 Pakuti mkulu wa ansembe ali yense, wotengedwa mwa anthu, amaikika cifukwa ca anthu m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke mitulo, ndiponso nsembe, cifukwa ca macimo:
2 akhale wokhoza kumva cifundo ndi osadziwa ndi olakwa, popeza iye yekhanso amazingwa ndi cifoko;
3 ndipo cifukwa caceco ayenera, monga m'malo a anthuwo, moteronso m'malo a iye yekha, kupereka nsembe cifukwa ca macimo.
4 Ndipo palibe munthu adzitengera ulemuwo mwini wace, komatu iye amene aitanidwa ndi Mulungu, monga momwenso Aroni.
5 Koteronso Kristu sanadzilemekeza yekha ayesedwe Mkuluwansembe, komatu iye amene analankhula kwa iye,Mwana wanga ndi Iwe, Lero Ine ndakubala Iwe;
6 Monga anenanso mwina,Iwe ndiwe wansembe wa nthawizonseMonga mwa dongosolo la Melikizedeke.
7 Ameneyo, m'masiku a thupi lace anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukuru ndi misozi kwa iye amene anakhoza kumpulumutsa iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,