2 cifukwa ca coonadi cimene cikhala mwa ife, ndipo cidzakhala ndi ife ku nthawi yosatha:
3 Cisomo, cifundo, mtendere zikhale ndi ife zocokera kwa Mulungu Atate, ndi kwa Yesu Kristu Mwana wa Atate, m'coonadi ndi m'cikondi.
4 Ndakondwera kwakukuru kuti ndapeza ena a ana anu alikuyenda m'coonadi, monga tinalandira lamulo locokera kwa Atate.
5 Ndipo tsopano ndikupemphani, mkazi womveka inu, wosati monga kukulemberani lamulo latsopano, koma lomwelo tinali nalo kuyambira paciyambi, kuti tikondane wina ndi mnzace.
6 Ndipo cikondi ndi ici, kuti tiyende monga mwa malamulo ace. Ili ndi lamulolo, monga mudalimva kuyambira paciyambi, kuti mukayende momwemo.
7 Pakuti onyenga ambiri adaturuka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene sabvomereza kuti Yesu Kristu anadza m'thupi, Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Kristu.
8 Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazicita, koma kuti mulandire mphotho yokwanira.