11 Wokondedwa, usatsanza ciri coipa komatu cimene ciri cokoma. Iye wakucita cokoma acokera kwa Mulungu; ye wakucita coipa sanamuona Mulungu.
12 Demetriyo, adamcitira umboni anthu onse, ndi coonadi comwe; ndipo ifenso ticita umboni; ndipo udziwa kuti umboni wathu uli woona.
13 Ndinali nazo zambiriza kukulembera, komatu sindifuna kukulembera ndi kapezi ndi peni;
14 koma ndiyembekeza kukuona iwe msanga, ndipo tidzalankhula popenyana, Mtendere ukhale nawe. Akulankhula abwenzi, Lankhula abwenzi ndi kuchula maina ao.