2 Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera,
3 Pakuti ndinakondwera kwakukuru, pofika abale ndi kucita umboni za coonadi cako, monga umayenda m'coonadi.
4 Ndiribe cimwemwe coposa ici, cakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m'coonadi.
5 Wokondedwa, ucita cokhulupirika naco ciri conse, uwacitira abale ndi alendo omwe;
6 amene anacita umboni za cikondi cako pamaso pa Mpingo; ngati uwaperekeza amenewo pa ulendo wao koyenera Mulungu, udzacita bwino:
7 pakuti cifukwa ca dzinali anaturuka, osalandira kanthu kwa amitundu.
8 Cifukwa cace ife tiyenera kulandira otere, kuti tikakhale othandizana naco coonadi,