8 Cifukwa cace ife tiyenera kulandira otere, kuti tikakhale othandizana naco coonadi,
9 Ndalemba kanthu kwa Mpingo; komatu Diotrefe uja, wofuna kukhala wamkuru wa iwo, satilandira ife.
10 Momwemo, ndikadza ine, ndidzakumbutsa nchito zace zimene aeitazi, zakunena zopanda pace pa ife ndi mau oipa; ndipopopeza izi sizimkwanira, salandira abale iye yekha, ndipo ofuna kuwalandira awaletsa, nawataya kunja powaturutsa mu Mpingo,
11 Wokondedwa, usatsanza ciri coipa komatu cimene ciri cokoma. Iye wakucita cokoma acokera kwa Mulungu; ye wakucita coipa sanamuona Mulungu.
12 Demetriyo, adamcitira umboni anthu onse, ndi coonadi comwe; ndipo ifenso ticita umboni; ndipo udziwa kuti umboni wathu uli woona.
13 Ndinali nazo zambiriza kukulembera, komatu sindifuna kukulembera ndi kapezi ndi peni;
14 koma ndiyembekeza kukuona iwe msanga, ndipo tidzalankhula popenyana, Mtendere ukhale nawe. Akulankhula abwenzi, Lankhula abwenzi ndi kuchula maina ao.