17 Ngati tsono undiyesa woyanjana nawe, umlandire iye monga ine mwini.
18 Koma ngati anakulakwira kanthu, kapena wakongola kanthu, undiwerengere ine kameneko;
19 Ine Paulo ndicilemba ndi dzanja langa, ndidzacibwezera ine; kuti ndisanene nawe kuti iwe ndiwe mangawa anga.
20 Inde, mbale, ndikondwere nawe mwa Ambuye: utsitsimutse mtima wanga mwa Kristu.
21 Pokhulupirira kumvera kwako ndikulembera iwe, podziwa kuti udzacicanso koposa cimene ndinena.
22 Koma undikonzerenso pogona; pakuti ndiyembekeza kuti mwa mapemphero anu ndidzapatsidwa kwa inu.
23 Epafra wandende mnzanga mwa Kristu Yesu akulankhula iwe;