3 Cisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Kristu.
4 Ndiyamika Mulungu wanga nthawi zonse, ndi kukumbukila iwe m'mapemphero anga,
5 pakumva za cikondi cako ndi cikhulupiriro uli naco cakulinga kwa Ambuye Yesu, ndi kwa oyera mtima onse;
6 kuti ciyanjano ca cikhulupiriro cako cikakhale camphamvu podziwa cabwino ciri conse ciri mwa inu, ca kwa Kristu.
7 Pakuti ndinali naco cimwemwe cambiri ndi cisangalatso pa cikondi cako, popeza mitima ya oyera mtima yatsitsimuka mwa iwe, mbale.
8 Momwemo, ndingakhale ndiri nako kulimbika mtima kwakukuru m'Kristu kukulamulira cimene ciyenera,
9 koma makamaka ndidandaulira mwa cikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Kristu Yesu;