5 pakumva za cikondi cako ndi cikhulupiriro uli naco cakulinga kwa Ambuye Yesu, ndi kwa oyera mtima onse;
6 kuti ciyanjano ca cikhulupiriro cako cikakhale camphamvu podziwa cabwino ciri conse ciri mwa inu, ca kwa Kristu.
7 Pakuti ndinali naco cimwemwe cambiri ndi cisangalatso pa cikondi cako, popeza mitima ya oyera mtima yatsitsimuka mwa iwe, mbale.
8 Momwemo, ndingakhale ndiri nako kulimbika mtima kwakukuru m'Kristu kukulamulira cimene ciyenera,
9 koma makamaka ndidandaulira mwa cikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Kristu Yesu;
10 ndikudandaulira cifukwa ca mwana wanga, amene ndambala m'ndende, Onesimo,
11 amene kale sanakupindulira, koma tsopano watipindulira bwino iwe ndi ine;