7 Pakuti ndinali naco cimwemwe cambiri ndi cisangalatso pa cikondi cako, popeza mitima ya oyera mtima yatsitsimuka mwa iwe, mbale.
8 Momwemo, ndingakhale ndiri nako kulimbika mtima kwakukuru m'Kristu kukulamulira cimene ciyenera,
9 koma makamaka ndidandaulira mwa cikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Kristu Yesu;
10 ndikudandaulira cifukwa ca mwana wanga, amene ndambala m'ndende, Onesimo,
11 amene kale sanakupindulira, koma tsopano watipindulira bwino iwe ndi ine;
12 amene ndi yemweyo ndakubwezera iwe, ndiye mtima weni weni wa ine.
13 Ameneyo ndikadafuna ine kumsunga akhale nane, kuti m'malo mwako akadanditumikira ine m'ndende za Uthenga Wabwino: