1 CAKA caciwiri ca mfumu Dariyo, mwezi wacisanu ndi cimodzi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri kwa Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ciwanga ca Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kuti,
2 Atero Yehova wa makamu, akuti, Anthu awa anena, Nthawi siinafike, nthawi yakumanga nyumba ya Yehova.
3 Pamenepo mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti,
4 Kodi imeneyi ndiyo nthawi yakuti inu nokha mukhala m'nyumba zanu zocingidwa m'katimo, ndi nyumba iyi ikhale yopasuka?