Hagai 2 BL92

Ulemerero wa Kacisi waciwiri

1 Mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku la makumi awiri ndi cimodzi la mweziwo, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti,

2 Unenetu kwa Zerubabele, mwana wa Sealitiyeli, ciwanga ca Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkuru wa ansembe, ndi kwa otsala a anthu, kuti,

3 Adatsala ndani mwa inu amene anaona nyumba iyi m'ulemerero wace woyamba? ndipo muiona yotani tsopano? Kodi siikhala m'maso mwanu ngati cabe?

4 Koma limbika tsopano, Zerubabele, ati Yehova; ulimbikenso Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkuru wa ansembe; ndipo mulimbike inu nonse anthu a m'dziko, ati Yehova, ndi kucita; pakui. Ine ndiri pamodzi ndi inu, ati Yehova wa makamu;

5 monga momwe ndinapangana nanu muja munaturuka m'Aigupto, ndi Mzimu wanga unakhala pakati pa inu; musamaopa inu.

6 Pakuti atero Yehova wa makamu: Kamodzinso, katsala kanthawi, ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi mtunda womwe;

7 ndipo ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu.

8 Siliva ndi wanga, golidi ndi wanga, ati Yehova wa makamu.

9 Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo, ati Yehova wa makamu; ndipo m'malo muno ndidzapatsa mtendere, ati Yehova wa makamu.

Madzudzulo ndi malonjezo

10 Tsiku la makumi awiri ndi anai la mwezi wacisanu ndi cinai, caka caciwiri ca Dariyo, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti,

11 Atero Yehova wa makamu: Funsatu ansembe za cilamulo, ndi kuti,

12 Munthu akanyamulira nyama yopatulika m'ngudulira, nakhudza mkate, kapena ndiwo, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena cakudya ciri conse, ndi ngudulira, kodi cisandulika copatulika? Ndipo ansembe anayankha nati, Iai.

13 Pamenepo Hagai anati, Munthu wodetsedwa ndi mtembo akakhudza kanthu ka izi, kodi kali kodetsedwa kanthuka? Ndipo ansembe anayankha nati, Kadzakhala kodetsedwa.

14 Ndipo Hagai anayankha, nati, Momwemo anthu awa, ndi momwemo mtundu uwu pamaso panga, ati Yehova; ndi momwemo nchito iri yonse ya manja ao; ndi ici acipereka, ciri codetsedwa.

15 Ndipo tsono, samalirani, kuyambira lero ndi m'tsogolomo, kuti, kusanaikidwe mwala pa mwala m'Kacisi wa Yehova,

16 pamenepo ponse munthu akadza ku mulu woyenera miyeso makumi awiri, pali khumi yokha; munthu akadza ku coponderamo mphesa kudzatunga mbiya makumi asanu, pali makumi awiri okha.

17 Ndinakukanthani ndi cinsikwi ndi cinoni ndi matalala m'nchito zonse za manja anu, koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.

18 Musamalire, kuyambira lero ndi m'tsogolo, kuyambira tsiku la makumi awiri ndi cinai la mwezi wacisanu ndi cinai, kuyambira tsiku lija anamanga maziko a Kacisi wa Yehova, samalirani.

19 Kodi mbeu ikali m'nkhokwe? Ngakhale mpesa, ndi mkuyu, ndi khangaza ndi mzitona sizinabala; kuyambira lero lino ndidzakudalitsani.

Adaniadzaonongeka, adzerubabele adzakwezeka

20 Ndipo mau a Yehova anadza nthawi yaciwiri kwa Hagai tsiku la makumi awiri la mwezi, ndi kuti,

21 Nena ndi Zerubabele ciwanga ca Yuda, kuti, Ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi;

22 ndipo ndidzagubuduza mipando yacifumu ya maufumu, ndidzaononga mphamvu ya maufumu a amitundu; ndidzagubuduza magareta ndi iwo akuyendapo; ndi akavalo ndi apakavalo adzatsika, yense ndi lupanga la mbale wace.

23 Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzakutenga, Zerubabele mtumiki wanga, mwana wa Sealitiyeli, ati Yehova, ndi kuika iwe ngati mphete yosindikizira; pakuti ndakusankha, ati Yehova wa makamu.

Mitu

1 2