Zekariya 1 BL92

Mneneri adandaulira anthu Ayuda aleke zoipa zao

1 MWEZI wacisanu ndi citatu, caka caciwiri ca Dariyo, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido mneneri, ndi kuti,

2 Yehova anakwiya kwambiri ndi makolo anu.

3 Cifukwa cace uziti nao, Atero Yehova wa makamu: Bwererani kudza kwa Ine, ati Yehova wa makamu, ndipo Ine ndidzabwerera kudza kwa inu, ati Yehova wa makamu.

4 Musamakhala ngati makolo anu, amenie aneneri akale anawapfuulira, nd kuti, Atero Yehova wa makamu Bwereranitu kuleka njira zanu zoipa, ndi macitidwe anu oipa; ko ma sanamva, kapena klimvera Ine ati Yehova.

5 Makolo anu, ali kut iwowo? ndi alieneri, akhala nd moyo kosatha kodi?

6 Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeza makolo anu? ndipo anabwera, nati, Monga wno Yehova wa makamu analingirira kuticitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa macitidwe athu, momwemo anaticitira. Masomphenya oyamba: akavalo,

7 Tsiku la makumi awiri ndi cinai la mwezi wakhumi ndi cimodzi, ndiwo mwezi wa Segati, caka caciwiri ca Dariyo, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido mneneri, ndi kuti,

8 Ndinaona usiku, taonani, munthu woyenda pa kavalo wofiira, alikuima pakati pa mitengo yamcisu inali kunsi; ndi pambuyo pace panali akavalo ofiira, odera ndi oyera.

9 Pamenepo ndinati, Awa ndi ciani, mbuyanga? Ndi mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, Ndidzakuonetsa awa ndi ciani.

10 Ndipo wakuima pakati pa mitengo yamcisu anayankha, nati, Awa ndiwo amene Yehova anawatumiza ayendeyende m'dziko.

11 Ndipo iwo anamyankha mthenga wa Yehova wakuima pakati pa mitengo yamcisu, nati, Tayendayenda m'dziko, ndipo taonani, dziko lonse likhala cete, lipumula.

12 Ndipo mthenga wa Yehova anayankha nati, Yehova wa makamu, mudzakhala mpaka liti osacitira cifundo Yerusalemu, ndi midzi ya Yuda, imene munakwiya nayo zaka izi makumi asanu ndi awiri?

13 Ndipo Yehova anamyankha mthenga wakulankhula ndi ine mau okoma, mau akutonthoza mtima.

14 Ndipo mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, Pfuula, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Ndicitira nsanje Yerusalemu ndi Ziyoni ndi nsanje yaikuru.

15 Ndipo ndikwiya nao amitundu okhala osatekeseka ndi mkwiyo waukuru; pakuti ndinakwiya pang'ono, ndipo anathandizira coipa,

16 Cifukwa cace atero Yehova: Ndabwera kudza ku Yerusalemu ndi zacifundo; nyumba yanga idzamangidwamo, ndipo adzayesa Yerusalemu ndi cingwe.

17 Pfuulanso, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Midzi yanga idzalemerera ndi kufalikiranso; ndipo Yehova adzasangalatsanso Ziyoni, nadzasankhamo Yerusalemu.

Masomphenya aciwiri: nyanga zinai ndi osula anai

18 Ndipo ndinakweza maso anga, ndinapenya, taonani, nyanga zinai.

19 Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Izi nziani? Ndipo anandiyankha, Izi ndi nyangazi zinabalalitsa Yuda, Israyeli, ndi Yerusalemu.

20 Ndipo Yehova anandionetsa osula anai.

21 Pamenepo ndinati, Adzeranji awa? Ndipo ananena, nati, Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, wopandanso wina woweramutsa mutu wace; koma awa anadza kuziopsa, kugwetsa nyanga za amitundu, amene anakwezera dziko la Yuda nyanga zao kulimwaza.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14