1 Pamenepo anandionetsa Yoswa mkulu wa ansembe alikuima pamaso pa mthenga wa Yehova, ndi Satana alikuima pa dzanja lace lamanja, atsutsana naye.
2 Ndipo Yehova anati kwa Satana, Yehova akudzudzula, Satana iwe; inde Yehova amene anasankha Yerusalemu akudzudzula; uyu sindiye muuni wofumulidwa kumoto?
3 Koma Yoswa analikubvala nsaru zonyansa, naima pamaso pa mthenga.
4 Ndipo Iye anayankha nanena ndi iwo akuima pamaso pace, ndi kuti, Mumbvule nsaru zonyansazi. Nati kwa iye, Taona, ndakucotsera mphulupulu zako, ndipo ndidzakubveka: zobvala za mtengo wace.
5 Ndipo ndinati, Amuike nduwira yoyera pamutu pace. Naika nduwira yoyera pamutu pace, nambveka ndi zobvala; ndi mthenga wa Yehova anaimirirapo,
6 Ndipo mthenga wa Yehova anamcitira Yoswa umboni, ndi kuti,
7 Atero Yehova wa makamu: Ukadzayenda m'njira zanga, ndi kusunga udikiro wanga, pamenepo udzaweruza nyumba yanga, ndi kusunga mabwalo anga, ndipo ndidzakupatsa malo oyendamo mwa awa oimirirapo.
8 Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo cizindikilo; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira.
9 Pakuti taona, mwalawo ndinauika pamaso pa Yoswa; pa mwala umodzi pali maso asanu ndi awiri; taonani, ndidzaloca malocedwe ace, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzacotsa mphulupulu ya dziko lija tsiku limodzi.
10 Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, mudzaitanizana yense mnansi wace patsinde pa mpesa ndi patsinde pa mkuyu.