1 Pamenepo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, taonani, mpukutu wouluka.
2 Ndipo anati kwa ine, Uona ciani? Ndipo ndinayankha, Ndiona mpukutu wouluka; utali wace mikono makumi awiri, ndi citando cace mikono khumi.
3 Ndipo anati kwa ine, Ili ndi temberero lirikuturukira pa dziko lonse; pakuti ali yense wakuba adzapitikitsidwa kuno monga mwa ili; ndi ali yense wakulumbira zonama adzapitikitsidwa kuno monga mwa ili.
4 Ndidzaliturutsa ili, ati Yehova wa makamu, ndipo lidzalowa m'nyumba ya wakuba, ndi m'nyumba ya iye wolumbira monama pa dzina langa; ndipo lidzakhala pakati pa nyumba yace, ndi kuitha pamodzi ndi mitengo yace ndi miyala yace.
5 Pamenepo mthenga wakulankhula ndi ine anaturuka, nati kwa ine, Kwezatu maso ako, nuone ngati nciani ici cirikuturukaci.
6 Ndipo ndinati, Nciani ici? Nati iye, Ici ndi efa alikuturuka. Natinso, Ici ndi maonekedwe ao m'dziko lonse;
7 (ndipo taonani, cozunguniza cantobvu cotukulidwa) ndipo ici ndi mkazi wokhala pakati pa efa.
8 Ndipo anati, Uyu ndi ucimo; namgwetsa m'kati mwa efa; naponya ntobvu wolemerawo pakamwa pace.
9 Pamenepo ndinakweza maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anaturuka akazi awiri, ndi m'mapiko mwao munali mphepo; ndipo anali nao mapiko ngati mapiko a cumba, nanyamula efayo pakati pa dziko ndi thambo.
10 Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Amenewa amuka naye kuti efayo?
11 Ndipo anati kwa ine, Kummangira nyumba m'dziko la Sinara; kuti amuike, namkhazikeko pa kuzika kwace.