1 Pemphani kwa Yehova mvula, m'nyengo ya mvula ya masika, kwa Yehova wolenga mphezi; ndipo adzawapatsa mibvumbi ya mvula, kwayense zophukira kuthengo.
2 Pakuti aterafi anena zopanda pace, ndi aula aona bodza; nafotokoza maloto acabe, asangalatsa nazo zopanda pace; cifukwa cace ayendayenda ngati nkhosa, azunzika popeza palibe mbusa.
3 Mkwiyo wanga wayakira abusa, ndipo ndidzalanga atonde; pakuti Yehova wa makamu adzazonda zoweta zace, ndizo nyumba ya Yuda, nadzaziika ngati kavalo wace waulemerero kunkhondo.
4 Kwa iye kudzafuma mwala wa kungondya, kwa iye msomali, kwa iye uta wankhondo, kwa iye osautsa onse pamodzi.
5 Ndipo adzakhala ngati ngwazi zakupondereza adani m'thope la kubwalo kunkhondo; ndipo adzacita nkhondo, cifukwa Yehova ali nao; ndi apakavalo adzacitidwa manyazi.
6 Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawacitira cifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataya konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera.
7 Ndipo iwo a ku Efraimu adzakhala ngati ngwazi, ndi mtima wao udzakondwera ngati ndi vinyo; ndipo ana ao adzaciona nadzakondwera; mtima wao udzakondwerera mwa Yehova.
8 Ndidzawayimbira mluzu ndi kuwasonkhanitsa, pakuti ndawaombola; ndipo adzacuruka monga anacurukira kale.
9 Ndipo ndidzawafesa mwa mitundu ya anthu, ndipo adzandikumbukila m'maiko akutali; nadzakhala pamodzi ndi ana ao, nadzabwera.
10 Ndidzawatenganso ku dziko la Aigupto, ndi kuwasonkhanitsa m'Asuri; ndipo ndidzalowa nao m'dziko la Gileadi ndi Lebano; koma sadzawafikira.
11 Ndipo adzapita pakati pa nyanja ya nsautso, nadzapanda mafunde a m'nyanja, ndi maiwe onse a mtsinje adzaphwa; ndi kudzikuza kwa Asuri kudzagwetsedwa; ndi ndodo yacifumu ya Aigupto idzacoka.
12 Ndipo ndidzawalimbitsa mwa Yehova; ndipo adzayendayendam'dzina lace, ati Yehova.