Zekariya 7 BL92

Kusala kosalamulidwa ndi Yehova

1 Ndipo kunacitika caka cacinai ca mfumu Dariyo, mau a Yehova anadza kwa Zekariya tsiku lacinai la mwezi wacisanu ndi cinai, ndiwo Kisilevi.

2 Ndipo a ku Beteli anatuma Sarezere ndi Regemeleke ndi anthu ao, apepeze Yehova,

3 nanene kwa ansembe a nyumba ya Yehova wa makamu, ndi kwa aneneri, ndi kuti, Kodi ndilire mwezi wacisanu, ndi kudzipatula, monga umo ndikacitira zaka izi zambiri?

4 Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti,

5 Nena kwa anthu onse a m'dziko, ndi kwa ansembe, kuti, Muja mukasala ndi kulira mwezi wacisanu, ndi wacisanu ndi citatu, zaka izi makumi asanu ndi awiri, kodi mukasalira Ine, Inedi?

6 Ndipo pamene mukadya, ndi pamene mukamwa, mukadya si ndinu, mukamwa si ndinu kodi?

7 Si ndiwo mau Yehova anawalalikira mwa aneneri oyamba aja, muja Yerusalemu anali nao okhalamo, ndi wokhazikika; ndi m'midzi mwace pozungulira pace, ndi m'dziko la kumwela, ndi m'cidikha munali anthu okhalamo?

8 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Zekariya, ndi kuti,

9 Watero Yehova wa makamu, kuti, Weruzani ciweruzo coona, nimucitire yense mnzace cifundo ndi ukoma mtima;

10 musazunza mkazi wamasiye, kapena ana amasiye, mlendo kapena waumphawi; ndipo nnena mmodzi wa inu alingirire m'mtima mwace kumcitira coipa munthu mnzace.

11 Koma anakana kumvera, nakaniza phewa lao, natseka makutu ao, kuti asamve.

12 Inde, anasanduliza mitima yao ikhale ngati mwala woti gwa, kuti angamve cilamulo, ndi mau amene Yehova wa makamu anatumiza ndi Mzimu wace mwa aneneri oyamba aja; m'menemo munafuma mkwiyo waukuru wocokera kwa Yehova wa makamu.

13 Ndipo kunacitika, monga Iye anapfuula, koma iwo sanamvera; momwemo iwo adzapfuula, koma Ine sindidzamva, ati Yehova wa makamu;

14 koma ndidzawabalalitsa ndi kabvumvulu mwa amitundu onse amene sanawadziwa. Motero dziko linakhala bwinja, m'mbuyo mwao; palibe munthu wopitapo ndi kubwererako; pakuti adaika dziko lofunikalo labwinja.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14