Zekariya 8 BL92

Madalitso olonjezedwa ndi Mulungu

1 Ndipo mau a Yehova wa makamui anadza kwa ine, ndi kuti,

2 Atero Yehova wa makamu: Ndimcitira nsanje Ziyoni ndi nsanje yaikuru, ndipo ndimcitira nsanje ndi ukali waukuru.

3 Atero Yehova: Ndabwerera kudza ku Ziyoni, ndidzakhala pakati pa Yerusalemu; ndi Yerusalemu adzachedwa, Madzi wa coonadi; ndi phiri la Yehova wa makamu, Phiri lopatulika.

4 Atero Yehova wa makamu: M'miseu ya Yerusalemu mudzakhalanso amuna ndi akazi okalamba, yense ndi ndodo yace m'dzanja lace cifukwa ca ukalamba wace.

5 Ndi m'miseu ya mudzi mudzakhala ana amuna ndi akazi akusewera m'miseu yace.

6 Atero Yehova wa makamu: Cikakhala codabwitsa pamaso pa otsala a anthu awa masiku awo, kodi cidzakhalanso codabwitsa pamaso panga? ati Yehova wa makamu.

7 Atero Yehova wa makamu: Taonani, ndidzapulumutsa anthu anga m'dziko la kum'mawa, ndi m'dziko la kumadzulo;

8 ndipo ndidzabwera nao, nadzakhala m'kati mwa Yerusalemu; ndipo iwo adzakhala anthu anga, nanenso ndidzakhala Mulungu wao, m'coonadi ndi m'cilungamo.

9 Atero Yehova wa makamu: Alimbike manja anu, inu akumva masiku ano mau awa pakamwa pa aneneri amene anakhalako tsiku lakuikidwa maziko a nyumba ya Yehova wa makamu, ndiyo Kacisi, kuti amangidwe.

10 Pakuti asanafike masiku aja, panalibe kulipidwira munthu, kapena kulipidwira nyama, ndipo analibe mtendere iye wakuturuka, kapena wakulowa, cifukwa ca wosautsa; pakuti ndinatumiza munthu yense atsutsane naye mnzace.

11 Koma tsopano sindidzakhala kwa otsala a anthu awa monga momwe ndinakhalira masiku oyamba, ati Yehova wa makamu.

12 Pakuti padzakhala mbeu ya mtendere; mpesa udzapatsa zipatso zace, ndi nthaka idzapatsa zobala zace, ndi miyamba Idzapatsa mame ao; ndipo ndidzalandiritsa otsala a anthu awa izi zonse, cikhale colowa cao.

13 Ndipo kudzacitika kuti, monga munali cotembereretsa mwa amitundu, inu nyumba ya Yuda, ndi nyumba ya Israyeli, momwemo ndidzakusungani, ndipo mudzakhala codalitsa naco; musaope, alimbike manja anu.

14 Pakuti atero Yehova wa makamu: Monga ndil nalingirira kucitira inu coipa, muja makolo anu anautsa mkwiyo wanga, ati Yehova wa makamu, ndipo sindinawaleka;

15 momwemonso ndinalingirira masiku ano kucitira cokoma Yerusalemu ndi nyumba ya Yuda; musaopa.

16 Izi ndizo muzicite: Nenani coonadi yense ndi mnzace; weruzani zoona ndi ciweruzo ca mtendere m'zipata zanu;

17 ndipo musalingirira coipa m'mtima mwanu yense pa mnzace; nimusakonde lumbiro lonama; pakuti izi zonse ndidana nazo, ati Yehova.

18 Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti,

19 Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wacinai, ndi kusala kwa mwezi wacisanu, ndi kusala kwa mwezi wacisanu ndi ciwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda cimwemwe ndi cikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; cifukwa cace kondani coonadi ndi mtendere.

20 Atero Yehova wa makamu: Kudzacitikanso kuti mitundu ya anthu, ndi okhalamo m'midzi yambiri adzafika,

21 ndi okhala m'mudzi umodzi adzamuka ku mudzi wina, ndi kuti, Tiyeni msanga kukapepeza Yehova, ndi kufunafuna Yehova wa makamu; ndimuka inenso.

22 Inde, mitundu yambiri ya anthu, ndi amitundu amphamvu adzadza kufunafuna Yehova wa makamu m'Yerusalemu, ndi kupepeza Yehova.

23 Atero Yehova wa makamu: Kudzacitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14