Zekariya 6 BL92

Masomphenya acisanu ndi citatu: magareta anai

1 Ndipo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anaturuka magareta anai pakati pa mapiri awiri; ndi mapiriwo ndiwo mapiri amkuwa.

2 Ku gareta woyamba kunali akavalo ofiira; ndi ku gareta waciwiri akavalo akuda;

3 ndi ku gareta wacitatu akavalo oyera; ndi ku gareta wacinai akavalo olimba amawanga.

4 Ndipo ndinayankha ndinati kwa mthenga wolankhula ndi ine, Izi nziani, mbuyanga?

5 Ndi mthenga anayankha, nati kwa ine, Izi ndi mphepo zinai zakumwamba zakuturuka kumene zimaimirira pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.

6 Gareta wa akavalo akuda aturukira ku dziko la kumpoto; ndi oyerawo aturukira kuwatsata; ndi amawanga aturukira ku dziko la kumwela.

7 Ndi amphamvuwo anaturuka nayesa kumka kuyendayenda m'dziko; pakuti adati, Mukani, yendayendani m'dziko. Momwemo anayendayenda m'dziko.

8 Ndipo anandiitana, nanena nane, kuti, Taonani, iwo akuturuka kumka ku dziko la kumpoto anapumulitsa Mzimu wanga m'dziko lakumpoto.

Akorona a Yoswa

9 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, ndi kuti,

10 Tenga a iwo a kundende, a Keledai, a Tobiya, ndi a Yedaya; nudze tsiku lomwelo, nulowe ku nyumba ya Yosiya, mwana wa Zefaniya, kumene anafikirako kucokera ku Babulo,

11 ndipo utenge siliva ndi golidi, nupange akorona, nuwaike pamutu pa Yoswa mwana wa Yehozadaki mkuru wa ansembe;

12 nunene naye, kuti, Atero Yehova wa makamu, ndi kuti, Taonani, munthu dzina lace ndilo Mphukira, ndipo adzaphuka m'malo mwace, nadzamanga Kacisi wa Yehova:

13 inde adzamanga Kacisi wa Yehova; nadzasenza ulemererowo, nadzakhala ndi kulamulira pa mpando wacifumu wace; nadzakhala wansembe pampando wacifumu wace; ndi uphungu wa mtendere udzakhala pakati pa iwo awiri,

14 Ndipo akorona adzakhala wa Kelemu, ndi wa Tobiya, ndi wa Yedaya, ndi wa Keni mwana wa Zefaniya, akhale cikumbutso m'Kacisi wa Yehova.

15 Ndipo iwo akukhala kutari adzafika, nadzamanga ku Kacisi wa Yehova, ndipo inu mudzadziwa kuti Yehova wa makamu ananditumiza kwa inu. Ndipo ici cidzacitika ngati mudzamvera mwacangu mau a Yehova Mulungu wanu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14