Zekariya 11 BL92

Kulangidwa kwa osalapa

1 Tsegula pa makomo ako Lebano, kuti moto uthe mikungudza yako.

2 Cema, mtengo wamlombwa, pakuti mkungudza wagwa, popeza mitengo yokoma yaipitsidwa; cemani athundu a ku Basani, pakuti nkhalango yocinjirizika yagwa pansi.

3 Mau a kucema kwa abusa! pakuti ulemerero wao waipsidwa; mau a kubangula kwa misona ya mikango! pakuti kudzikuza kwa Yordano kwaipsidwa.

4 Atero Yehova Mulungu wanga: Dyetsani zoweta zakukaphedwa;

5 zimene eni ace azipha, nadziyesera osaparamula; ndi iwo akuwagulitsa akuti, Alemekezedwe Yehova, pakuti ine ndine wolemera; ndi abusa ao sazicitira cifundo.

6 Pakuti sindidzacitiranso cifundo okhala m'dzikomo, ati Yehova; koma taonani, ndidzapereka anthu, yense m'dzanja la mnansi wace, ndi m'dzanja la mfumu yace; ndipo iwo adzakantha dzikoli, ndi m'dzanja mwao sindidzawalanditsa.

7 M'mwemo ndinadyetsa zoweta zakukaphedwa, ndizo zoweta zonyankhalala. Ndipo ndinadzitengera ndodo ziwiri; yina ndinaicha Cisomo, inzace ndinaicha Comanganitsa; ndipo ndinadyetsa zowetazo.

8 Ndipo ndinatha abusa atatuwo mwezi umodzi; pakuti mtima wanga unalema nao, ndi mtima waonso unaipidwa nane.

9 Pamenepo ndinati, Sindidzadyetsanso inu; cirikufa cife; cosoweka cisoweke; ndi zotsala zidyane, conse nyama ya cinzace.

10 Ndipo ndinatenga ndodo yanga Cisomo, ndi kuidula pakati, kuti ndiphwanye pangano langa ndinalicita ndi mitundu yonse ya anthu.

11 Ndipo linatyoka tsikulo, momwemo zonyankhalala za zoweta, zakundisamalira Ine, zinadziwa kuti ndiwo mau a Yehova.

12 Ndipo ndinanena nao, Cikakomera inu, ndipatseni mphotho yanga; ngati iai, lekani. Ndipo anayesa mphotho yanga, kulemera kwace ndarama zasiliva makumi atatu.

13 Ndipo Yehova anati kwa ine, Kaziponye kwa woumba mbiya, mtengo wace wokometsetsa anandiyesawo. Ndipo ndinatenga ndarama makumi atatu asiliva, ndi kuziponya kwa woumba mbiya, m'nyumba ya Yehova.

14 Pamenepo ndinadula ndodo yanga yina, ndiyo Comanganitsa, kuti ndithetse cibale ca pakati pa Yuda ndi Israyeli.

15 Ndipo Yehova anati kwa ine, Dzitengerenso zipangizo za mbusa wopusa.

16 Pakuti taonani, ndidzautsa mbusa m'dziko amene sadzazonda otayika, kapena kufunafuna zomwazika, kapena kulunzitsa yotyoka, kapena kudyetsa yamoyo, koma adzadya nyama ya zonenepa, nadzang'amba ziboda zao.

17 Tsoka mbusa wopanda pace, wakusiya zoweta! lupanga pa dzanja lace, ndi pa diso lace la kumanja; dzanja lace lidzauma konse, ndi diso lace lamanja lidzada bii.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14