Habakuku 2 BL92

Akasidi omwe adzalangidwa

1 Ndidzaima pa dindiro langa ndi kudziika palinga, ndipo ndidzayang'anira ndione ngati adzanenanji mwa ine, ngatinso ndidzamyankha ciani pa coneneza canga.

2 Ndipo Yehova anandiyankha nati, Lembera masomphenyawo, nuwacenutse pamagome, kuti awawerenge mofulumira.

3 Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pace, osanama; akacedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.

4 Taonani, moyo wace udzikuza, wosaongoka m'kati mwace; koma wolungama adzakhala ndi moyo mwa cikhulupiriro cace.

5 Ndiponso vinyo ngwonyenga, ngati munthu wodzikuza, wosakhala kwao; wakukulitsa cikhumbo cace ngati kunsi kwa manda, akunga imfa, yosakhuta, koma adzisonkhanitsira amitundu onse, nadzimemezera mitundu yonse ya anthu.

6 Kodi sadzamnenera fanizo onsewo, ndi mwambi womnyodola, ndi kuti, Tsoka iye wocurukitsa zimene siziri zace! mpaka liti? iye wodzisenzera zigwiriro.

7 Sadzauka kodi modzidzimuka iwo amene adzakuluma, ndi kugalamuka iwo amene adzakugwedezetsa; ndipo udzakhala zofunkha zao?

8 Popeza iwe wafunkha amitundu ambiri, otsala onse a mitundu ya anthu adzakufunkha iwe; cifukwa ca mwazi wa anthu, ndi ciwawa cocitikira dziko, mudzi, ndi onse okhalamo.

9 Tsoka iye wakupindulitsira nyumba yace phindu loipa, kuti aike cisanja cace ponyamuka, kuti alanditsidwe m'dzanja la coipa!

10 Wapangira nyumba yako camanyazi, pakuononga mitundu yambiri ya anthu, ndipo wacimwira moyo wako.

11 Pakuti mwala wa m'khoma upfuula, ndi mtanda wa kuphaso udzaubvomereza.

12 Tsoka tye wakumanga mudzindi mwazi, nakhazikitsa mudzi ndi cisalungamo!

13 Taonani, sicicokera kwa Yehova wa makamu kodi kuti mitundu ya anthu ingogwirira moto nchito, ndi anthu angodzilemetsa pa zopanda pace?

14 Pakuti dziko lapansi lidzadzazidwa ndi cidziwitso ca ulemerero wa Yehova, monga madzi aphimba pansi panyanja.

15 Tsoka wakuninkha mnzace cakumwa, ndi kuonjezako mankhwala ako, ndi kumledzeretsa, kuti upenyerere manyazi ao!

16 Udzazidwa nao manyazi m'malo mwa ulemerero; imwa iwenso, nukhale wosadulidwa; cikho ca dzanja lamanja la Yehova cidzatembenukira iwe, ndi kusanza kwa manyazi kudzakhala pa ulemerero wako,

17 Pakuti ciwawa cidacitikira Lebano cidzakukuta, ndi cionongeko ca nyama cidzakuopsa; cifukwa ca mwazi wa anthu, ndi ciwawa cocitidwira dziko, mudzi, ndi onseokhalamo.

18 Apindulanji nalo fano losema, kuti wakulipanga analisema; fano loyenga ndi mphunzitsi wamabodza, kuti wakulipanga alikhulupirira, ata panga matafano osanena mau?

19 Tsoka iye wakunena kwa mtengo, Galamuka; ndi kwa mwala wosalankhula, Nyamuka Kodi ici ciphunzitsa? Taona cakutidwa ndi golidi ndi siliva, ndi m'kati mwace mulibe mpweya konse.

20 Koma Yehova ali m'Kacisi wace wopatulika; dziko lonse lapansi ale, cete pamaso pace.

Mitu

1 2 3