Habakuku 3 BL92

Pemphero la Habakuku

1 Pemphero la Habakuku mneneri, pa Sigionoto.

2 Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha;Yehova, tsitsimutsani nchito yanu pakati pa zaka,Pakati pa zaka mudziwitse;Pa mkwiyo mukumbukile cifundo.

3 Mulungu anafuma ku Temani,Ndi Woyerayo ku phiri la Parana.Ulemerero wace unaphimba miyamba,Ndi dziko lapansi linadzala ndi kumlemekeza.

4 Ndi kunyezimira kwace kunanga kuunika;Anali nayo mitsitsi ya dzuwa yoturuka m'dzanja lace.Ndi komweko kunabisika mphamvu yace.

5 Patsogolo pace panapita mliri,Ndi makara amoto anaturuka pa mapaziace.

6 Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi;Anapenya, nanjenjemeretsa amitundu;Ndi mapiri acikhalire anamwazika,Zitunda za kale lomwe zinawerama;Mayendedwe ace ndiwo a kale lomwe.

7 Ndinaona mahema a Kusani ali mkusauka;Nsaru zocinga za dziko la Midyani zinanjenjemera.

8 Kodi Yehova anaipidwa nayo mitsinje?Mkwiyo wanu unali pamitsinje kodi,Kapena ukali wanu panyanja,Kuti munayenda pa akavalo anu,Pa magareta anu a cipulumutso?

9 Munapombosola uta wanu;Malumbiro analumbirira mafuko anali mau oona.Munang'amba dziko lapansi ndi mitsinje.

10 Mapiri anakuonani, namva zawawa;Cigumula ca madzi cinapita;Madzi akuya anamveketsa mau ace,Nakweza manja ace m'mwamba.

11 Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao;Pa kuunika kwa mibvi yanu popita iyo.Pa kung'anipa kwa nthungo yanu yonyezimira.

12 Munaponda dziko ndi kulunda,Munapuntha amitundu ndi mkwiyo.

13 Munaturukira cipulumutso ca anthu anu,Cipulumutso ca odzozedwa anu;Munakantha mutu wa nyumba yawoipa,Ndi kufukula maziko kufikira m'khosi.

14 Munapyoza ndi maluti ace mutu wa ankhondo ace;Anadza ngati kabvumvulu kundimwaza;Kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mabisika.

15 Munaponda panyanja ndi akavaloanu,Madzi amphamvu anaunjikana mulu.

16 Ndinamva, ndi m'mimba mwanga munabwadamuka,Milomo yanga inanthunthumira pamau,M'mafupa mwanga mudalowa cibvundi, ndipo ndinanjenjemera m'malo mwanga;Kuti ndipumule tsiku lamsauko,Pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu.

17 Cinkana mkuyu suphuka,Kungakhale kulibe zipatso kumpesa;Yalephera nchito ya azitona,Ndi m'minda m'mosapatsa cakudya;Ndi zoweta zacotsedwa kukhola,Palibenso ng'ombe m'makola mwao;

18 Koma ndidzakondwera mwa Yehova,Ndidzasekerera mwa Mulungu wa cipulumutso canga.

19 Yehova, Ambuye, ndiye mphamvuyanga,Asanduliza mapazi anga ngati a mbawala,Nadzandipondetsa pa misanje yanga.

Mitu

1 2 3