Zefaniya 1 BL92

Mau oopsa akucenjeza Yerusalemu ndi Yuda

1 MAU a Yehova amene anadza kwa Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya, masiku a Yosiya, mwana wa Amoni mfumu ya Yuda.

2 Kuzitha ndidzazitha zonse kuzicotsa panthaka, ati Yehova.

3 Ndidzatha munthu ndi nyama; ndidzatha mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja, ndi zokhumudwitsa pamodzi ndi oipa; ndipo ndidzaononga anthu kuwacotsa panthaka, ati Yehova.

4 Ndipo ndidzatambasulira dzanja langa pa Yuda, ndi pa onse okhala m'Yerusalemu; ndipo a ndidzaononga otsala a Baala kuwacotsa m'malo muno, ndi dzina la Akemari pamodzi ndi ansembe;

5 ndi iwo akulambira khamu la kumwamba pamwamba pa matsindwi; ndi iwo akulambira, akulumbira pali Yehova, nalumbiranso pali mfumu;

6 ndi iwo akubwerera osamtsata Yehova; ndi osamfuna Yehova, kapena kufunsira kwa Iye.

7 Khala cete pamaso pa Ambuye Yehova; pakuti tsiku la Yehova liyandikira; pakuti Yehova wakonzeratu nsembe, anapatula oitanidwa ace.

8 Ndipo kudzacitika tsiku la nsembe ya Yehova, kuti ndidzalanga akalonga ndi ana a mfumu, ndi onse akubvala cobvala cacilendo.

9 Ndipo tsiku ilo ndidzalanga olumpha ciundo, nadzaza nyumba ya mbuye wao ndi ciwawa ndi cinyengo.

10 Ndipo tsiku ilo, ati Yehova, kudzakhala phokoso lakulira locokera ku cipata cansomba, ndi kucema kocokera ku dera laciwiri, ndi kugamuka kwakukuru kocokera kuzitunda.

11 Cemani okhala m'cigwa, pakuti amalonda onse atayika, onsewo osenza siliva aonongeka.

12 Ndipo kudzacitika nthawi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m'mtima mwao, Yehova sacita cokoma, kapena kucita coipa.

13 Ndipo zolemera zao zidzakhala zakufunkhidwa; ndi nyumba zao zabwinja; adzamangadi nyumba, koma sadzagonamo; adzanka minda yampesa koma sadzamwa vinyo wace.

14 Tsiku lalikuru la Yehova liri pafupi, liri pafupi lifulumira kudza, mau a tsiku la Yehova; munthu wamphamvu adzalirapo mowawa mtima.

15 Tsikulo ndi tsiku la mkwiyo, tsiku la msauko ndi lopsinja tsiku la bwinja, ndi cipasuko, tsiku la mdima ndi la cisisira, tsiku la mitambo ndi lakuda bii;

16 tsiku la lipenga ndi lakupfuulira midzi yamalinga, ndi nsanja zazitali za kungondya.

17 Ndipo ndidzatengera anthu zowapsinja, kuti adzayenda ngati anthu a'khungu, popeza anacimwira Yehova; ndi mwazi wao udzatsanulidwa ngati pfumbi, ndi nyama yao idzanga ndowe.

18 Ngakhale siliva wao, ngakhale golidi wao sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yace; pakuti adzacita cakutsiriza, mofulumira, onse okhala m'dziko.

Mitu

1 2 3