1 Tsoka uyo wopanduka, ndi wodetsedwa, ndiye mudzi wozunza!
2 Sanamvera mau, sanalola kulangizidwa; sanakhulupirira Yehova, sanayandikira kwa Mulungu wace.
3 Akalonga ace m'kati mwace ndiwo mikango yobangula; oweruza ace ndi mimbulu ya madzulo, sasiya kanthu ka mawa.
4 Aneneri ace ndiwo anthu a matukutuku ndi onyenga; ansembe ao anaipsa malo opatulika, napotoza cilamulo.
5 Yehova pakati pace ali wolungama; sadzacita cosalungama, m'mawa ndi m'mawa aonetsera ciweruzo cace poyera, cosasowa kanthu; koma wosalungama sadziwa manyazi.
6 Ndaononga amitundu; nsanja zao za kungondya nza bwinja, ndapasula miseu yao, palibe wopitapo; midzi yao yaonongeka, palibe munthu, palibe wokhalamo.
7 Ndinati, Zedi udzandiopa Ine, udzalola kulangizidwa, kuti pokhala pace pasaonongeke, monga mwa zonse ndamuikira; koma analawirira mamawa, nabvunditsa macitidwe ao onse.
8 Cifukwa cace, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.
9 Pakuti pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera, kuti onsewa aitanire pa dzina la Yehova kumtumikira ndi mtima umodzi.
10 Kucokera tsidya lija la mitsinje ya Kusi ondipembedza, ndiwo mwana wamkazi wa obalalika anga, adzabwera naco copereka canga.
11 Tsiku ilo sudzacita manyazi ndi zocita zako zonse unandilakwira nazo; pakuti pamenepo ndidzacotsa pakati pako amene akondwera ndi kudzikuza kwako, ndipo sudzacita kudzikuzanso m'phiri langa lopatulika.
12 Koma ndidzasiya pakati pako anthu ozunzika ndi osauka, ndipo iwo adzakhulupirira dzina la Yehova.
13 Otsala a Israyeli sadzacita cosalungama, kapena kunena mabodza; ndi m'kamwa mwao simudzapezeka lilime lonyenga; pakuti adzadya nadzagona pansi, ndi palibe wakuwaopsa.
14 Yimba, mwana wamkazi wa Ziyoni; pfuula, Israyeli; kondwera nusekerere ndi mtima wonse, mwana wamkazi wa Yerusalemu.
15 Yehova wacotsa maweruzo ako, anataya kunja mdani wako; mfumu ya Israyeli, Yehova, ali pakati pako, sudzaopanso coipa.
16 Tsiku lomwelo adzati kwa Yerusalemu, Usaopa Ziyoni, manja anu asakhale olefuka.
17 Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi cimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'cikondi cace; adzasekerera nawe ndi kuyimbirapo.
18 Ndidzasonkhanitsa iwo akulirira msonkhano woikika, ndiwo a mwa iwe, amene katundu wace anawakhalira mtonzo.
19 Taonani, nthawi yomweyo ndidzacita nao onse akuzunza iwe; ndipo ndidzapulumutsa wotsimphinayo, ndi kusonkhanitsa wopitikitsidwayo; ndipo ndidzawaika akhale cilemekezo ndi dzina, iwo amene manyazi ao anali m'dziko lonse.
20 Nthawi yomweyo ndidzakulowetsani, ndi nthawi yomweyo ndidzakusonkhanitsani; pakuti ndidzakuikani mukhale dzina, ndi cilemekezo mwa mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi, pamene ndibweza undende wanu pamaso panu, ati Yehova.