3 Pamenepo mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti,
4 Kodi imeneyi ndiyo nthawi yakuti inu nokha mukhala m'nyumba zanu zocingidwa m'katimo, ndi nyumba iyi ikhale yopasuka?
5 Cifukwa cace tsono, atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu.
6 Mwabzala zambiri, koma mututa pang'ono; mukudya, koma osakhuta; mukumwa, koma osakoledwa; mudzibveka, koma palibe wofundidwa; ndi iye wolembedwa nchito yakulipidwa alandirira kulipirako m'thumba lobooka.
7 Atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu.
8 Kwerani ku dziko la mapiri, ndi kukwera nayo mitengo, nimumange nyumbayi; ndipo kudzandikomera, ndipo ndidzalemekezedwa, ati Yehova.
9 Munayembekezera zambiri, koma taonani, pang'ono; ndipo, mutabwera napo kwanu, ndinauzirapo. Cifukwa ninji? ati Yehova wa makamu. Cifukwa ca nyumba yanga yokhala yopasuka, ndipo nuthamangira yense kunyumba kwace.