2 Unenetu kwa Zerubabele, mwana wa Sealitiyeli, ciwanga ca Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkuru wa ansembe, ndi kwa otsala a anthu, kuti,
3 Adatsala ndani mwa inu amene anaona nyumba iyi m'ulemerero wace woyamba? ndipo muiona yotani tsopano? Kodi siikhala m'maso mwanu ngati cabe?
4 Koma limbika tsopano, Zerubabele, ati Yehova; ulimbikenso Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkuru wa ansembe; ndipo mulimbike inu nonse anthu a m'dziko, ati Yehova, ndi kucita; pakui. Ine ndiri pamodzi ndi inu, ati Yehova wa makamu;
5 monga momwe ndinapangana nanu muja munaturuka m'Aigupto, ndi Mzimu wanga unakhala pakati pa inu; musamaopa inu.
6 Pakuti atero Yehova wa makamu: Kamodzinso, katsala kanthawi, ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi mtunda womwe;
7 ndipo ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu.
8 Siliva ndi wanga, golidi ndi wanga, ati Yehova wa makamu.