1 Pamenepo Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wace ali m'mimba mwa nsombayo.
2 Ndipo anati,Ndinaitana Yehova m'nsautso yanga,Ndipo anandiyankha ine;Ndinapfuula ndiri m'mimba ya manda,Ndipo munamva mau anga.
3 Pakuti munandiponya mwakuya m'kati mwa nyanja,Ndipo madzi anandizinga;Mapfunde anu onse a nyondonyondo anandimiza.
4 Ndipo ndinati, Ndatayika ndicoke pamaso panu;Koma ndidzapenyanso Kacisi wanu wopatulika.