1 Pamenepo Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wace ali m'mimba mwa nsombayo.
2 Ndipo anati,Ndinaitana Yehova m'nsautso yanga,Ndipo anandiyankha ine;Ndinapfuula ndiri m'mimba ya manda,Ndipo munamva mau anga.
3 Pakuti munandiponya mwakuya m'kati mwa nyanja,Ndipo madzi anandizinga;Mapfunde anu onse a nyondonyondo anandimiza.
4 Ndipo ndinati, Ndatayika ndicoke pamaso panu;Koma ndidzapenyanso Kacisi wanu wopatulika.
5 Madzi anandizinga mpaka moyo wanga,Madzi akuya anandizungulira,Kayandeyande wa m'nyanja anandikulunga mutu.
6 Ndinatsikira ku matsinde a mapiri,Mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha;Koma munandikwezera moyo wanga kuucotsa kucionongeko, Yehova Mulungu wanga.
7 Pokomoka moyo wanga m'kati mwanga ndinakumbukila Yehova;Ndi pemphero langa linafikira Inu m'Kacisi wanu wopatulika.
8 Iwo osamalira mabodza opanda paceAtaya cifundo cao cao.
9 Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika,Ndidzakwaniritsacowindacanga.Cipulumutso nca Yehova.
10 Pamenepo Yehova analankhula ndi nsombayo, ndipo inamsanzira Yona kumtunda.