Yona 4 BL92

Kudandaula kwa Yona, kumdzudzula kwa Mulungu

1 Koma sikudakomera Yona konse, ndipo anapsa mtima.

2 Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! si ndiwo mau anga ndikali m'dziko langa? cifukwa cace ndinafulumira kuthawira ku Tarisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wacisomo ndi wodzala cifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mocuruka, ndi woleka coipaco.

3 Ndipo tsopano, Yehova, mundicotseretu moyo wanga, kundikomera ine kufa, osakhala ndi moyo ai.

4 Ndipo Yehova anati, Uyenera kupsa mtima kodi?

5 Pamenepo Yona anaturuka m'mudzi, nakhala pansi kum'mawa kwa mudzi, nadzimangira komweko thandala, nakhala pansi pace mumthunzi mpaka adzaona cocitikira mudzi.

6 Ndipo Yehova Mulungu anaikiratu msatsi, naumeretsera Yona, ucite mthunzi pamutu pace, kumlanditsa m'nsautso yace. Ndipo Yona anakondwera kwambiri cifukwa ca msatsiwo.

7 Koma Mulungu anauikira mphanzi pakuca m'mawa mwace, ndiyo inadya msatsi, nufota.

8 Ndipo kunali, poturuka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum'mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wace wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai.

9 Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima cifukwa ca msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.

10 Ndipo Yehova anati, Unacitira cifundo msatsiwo umene sunagwirapo nchito, kapena kuumeretsa, umene unamera usiku, nutha usiku;

11 ndipo sindiyenera Ine kodi kucitira cifundo Nineve mudzi waukuru uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati pa dzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?

Mitu

1 2 3 4