1 Dzisanthuleni, inde santhulani; inu mtundu wosakhumba kanthu;
2 lamulo lisanabale, tsiku lisanapitirire ngati mungu, usanakugwereni mkwiyo waukali wa Yehova, lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova.
3 Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m'dziko, amene munacita ciweruzo cace; funani cilungamo, funani cifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.
4 Pakuti Gaza adzasiyidwa, ndi Asikeloni adzakhala bwinja; adzaingitsa Asidodi usana, ndi Ekroni adzazulidwa.
5 Tsoka, okhala m'dziko la kunyanja, mtundu wa Akereti! Mau a Yehova atsutsana nawe, Kanani, dziko la Afilisti; ndidzakuononga, kuti pasakhale wokhala m'dziko.
6 Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala husa, ndi mapanga a abusa, ndi makola a zoweta.