11 Yehova adzawakhalira woopsa; pakuti adzaondetsa milungu yonse ya pa dziko lapansi; ndipo adzamlambira Iye, yense pamalo pace, a m'zisumbu zonse za amitundu.
12 Inunso Akusi, mudzaphedwa ndi lupanga langa.
13 Ndipo adzatambasulira dzanja lace kumpoto nadzaononga Asuri, nadzasanduliza Nineve akhale bwinja, wouma ngati cipululu.
14 Ndipo zoweta zidzagona pansi pakati pace; nyama zonse za mitundu mitundu; ndi bvuo ndi nungu zidzakhala m'mitu ya nsanamira zace; adzayimba mau ao m'mazenera; paziundo padzakhala cipasuko; pakuti anagadamula nchito yace ya mkungudza.
15 Uwu ndi mudzi wosekererawo unakhala wosasamalira, unanena m'mtima mwace, Ine ndine, ndi wopanda ine palibe wina; ha! wasanduka bwinja, mogonera nyama za kuthengo! yense wakuupitirira adzatsonya mtsonyo, ndi kupukusa mutu.