12 Inunso Akusi, mudzaphedwa ndi lupanga langa.
13 Ndipo adzatambasulira dzanja lace kumpoto nadzaononga Asuri, nadzasanduliza Nineve akhale bwinja, wouma ngati cipululu.
14 Ndipo zoweta zidzagona pansi pakati pace; nyama zonse za mitundu mitundu; ndi bvuo ndi nungu zidzakhala m'mitu ya nsanamira zace; adzayimba mau ao m'mazenera; paziundo padzakhala cipasuko; pakuti anagadamula nchito yace ya mkungudza.
15 Uwu ndi mudzi wosekererawo unakhala wosasamalira, unanena m'mtima mwace, Ine ndine, ndi wopanda ine palibe wina; ha! wasanduka bwinja, mogonera nyama za kuthengo! yense wakuupitirira adzatsonya mtsonyo, ndi kupukusa mutu.