3 Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m'dziko, amene munacita ciweruzo cace; funani cilungamo, funani cifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.
4 Pakuti Gaza adzasiyidwa, ndi Asikeloni adzakhala bwinja; adzaingitsa Asidodi usana, ndi Ekroni adzazulidwa.
5 Tsoka, okhala m'dziko la kunyanja, mtundu wa Akereti! Mau a Yehova atsutsana nawe, Kanani, dziko la Afilisti; ndidzakuononga, kuti pasakhale wokhala m'dziko.
6 Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala husa, ndi mapanga a abusa, ndi makola a zoweta.
7 Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala la otsala a nyumba ya Yuda; adzadyetsa zoweta zao pamenepo; madzulo adzagona m'nyumba za Asikeloni; pakuti Yehova Mulungu wao adzawazonda, nadzabweza undende wao.
8 Ndinamva kutonza kwa Moabu ndi matukwano a ana a Amoni, zimene anatonza nazo anthu anga, ndi kudzikuza pa malire ao.
9 Cifukwa cace, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Zedi Moabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pocuruka khwisa ndi maenje a mcere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala amtundu wa anthu anga adzawalandira akhale colowa cao.