6 Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala husa, ndi mapanga a abusa, ndi makola a zoweta.
7 Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala la otsala a nyumba ya Yuda; adzadyetsa zoweta zao pamenepo; madzulo adzagona m'nyumba za Asikeloni; pakuti Yehova Mulungu wao adzawazonda, nadzabweza undende wao.
8 Ndinamva kutonza kwa Moabu ndi matukwano a ana a Amoni, zimene anatonza nazo anthu anga, ndi kudzikuza pa malire ao.
9 Cifukwa cace, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Zedi Moabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pocuruka khwisa ndi maenje a mcere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala amtundu wa anthu anga adzawalandira akhale colowa cao.
10 Ici adzakhala naco m'malo mwa kudzikuza kwao, cifukwa anatonza, nadzikuza pa anthu a Yehova wa makamu.
11 Yehova adzawakhalira woopsa; pakuti adzaondetsa milungu yonse ya pa dziko lapansi; ndipo adzamlambira Iye, yense pamalo pace, a m'zisumbu zonse za amitundu.
12 Inunso Akusi, mudzaphedwa ndi lupanga langa.