22 m'thupi lace mwa imfayo, kukaimika inu oyera, ndi opanda cirema ndi osatsutsika pamaso pace;
23 ngatitu mukhalabe m'cikhulupiriro, ocirimika ndi okhazikika ndi osasunthika kulekana naco ciyembekezo ca Uthenga Wabwino umene mudaumva, wolalikidwa colengedwa conse ca pansi pa thambo; umene ine Paulo ndakhala mtumiki wace.
24 Tsopano 1 ndikondwera nazo zowawazo cifukwa ca inu, ndipo 2 ndikwaniritsa zoperewera za cisautso ca Kristu m'thupi langa 3 cifukwa ca thupi lace, ndilo Eklesiayo;
25 amene ndinakhala mtumiki wace, 4 monga mwa udindo wa Mulungu umene anandipatsa ine wakucitira inti, wakukwaniritsa mau a Mulungu,
26 5 ndiwo cinsinsico cinabisika kuyambira pa nthawizo, ndi kuyambira pa mibadwoyo; koma anacionetsa tsopano kwa oyera mtima ace,
27 kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ici 6 cimene ciri cuma ca ulemerero wa cinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Kristu mwa inu, ciyembekezo ca ulemerero;
28 amene timlalikira ife, ndi kucenjeza munthu ali yense 7 ndi kuphunzitsa munthu ali yense mu nzeru zonse, 8 kuti tionetsere munthu ali yense wamphumphu mwa Kristu;