Akolose 3 BL92

Atsate kuyera-mtima, ndi cikondano ca pa abale

1 Cifukwa cace ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Kristu, funani zakumwamba, kumene kuli Kristu wokhala pa dzanja lamanja la Mulungu.

2 Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.

3 Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Kristu mwa Mulungu,

4 Pamene Kristu adzaoneka, ndiye moyo wathu, pamenepo inunso mudzaonekera pamodzi ndi iye m'ulemerero.

5 Cifukwa cace fetsani ziwalozo ziri padziko; dama, cidetso, cifunitso ca manyazi, cilakolako coipa, nelicisiriro, cimene ciri kupembedza mafano;

6 cifukwa ca izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;

7 zimene munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m'menemo,

8 Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zoturuka m'kamwa mwanu:

9 musamanamizana wina ndi mnzace; popeza mudabvula munthu wakale pamodzi ndi nchito zace,

10 ndipo munabvala watsopano, amene alikukonzekawatsopano, kuti akhale naco cizindikiritso, mousa mwa cifaniziro ca iye amene anamlenga iye;

11 pamene palibe Mhelene ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, wachedwa wakunja, Mskuti, kapolo, mfulu, komatu Kristu ndiye zonse, ndi m'zonse.

12 Cifukwa cace bvalani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wacifundo, kukoma mtima, kudzicepetsa, cifatso, kuleza mtima;

13 kulolerana wina ndi mnzace, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali naco cifukwa pa mnzace; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;

14 koma koposa izi zonse khalani naco cikondano, ndico comangira ca mtima wamphumphu.

15 Ndipo mtendere wa Kristu ucite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.

16 Mau a Knstu akhalitse mwa inu cicurukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndimayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuyimbira Mulungu ndi cisomo mumtima mwanu.

17 Ndipo ciri conse mukacicita m'mau kapena muncbito, citani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa iye.

Za banja la munthu

18 Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.

19 Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo.

20 Ana inu, mverani akubala inu m'zonse, pakuti ici Ambuye akondwera naco.

21 Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.

22 Akapolo inu, mverani m'zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, wosati ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu ndi mtima wakulinga kumodzi, akuopa Ambuye;

23 ciri conse mukacicita, gwirani nchito mocokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai;

24 podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya colowa; mutumikira Ambuye Kristu mwaukapolo.

25 Pakuti iye wakucita cosalungama adzalandiranso cosalungama anaeitaco; ndipo 1 palibe tsankhu.

Mitu

1 2 3 4