Akolose 4 BL92

1 Ambuye inu, citirani akapolo anu colungama ndi colingana; podziwa kuti inunso muli naye Mbuye m'Mwamba.

Awacenjeza za kupemphera ndi za kukhala nayo nzeru

2 Citani khama m'kupemphera, nimudikire momwemo ndi ciyamiko;

3 ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule cinsinsi ca Kristu; cimenenso ndikhalira m'ndende,

4 kuti ndicionetse ici monga ndiyenera kulankhula.

5 Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kucita macawi nthawi ingatayike.

6 Mau anu akhale m'cisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akarani.

Atumidwa Tukiko ndi Onesimo, Malankhulano

7 Zonse za kwa ine adzakuzindikiritsani Tukiko, mbale wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika ndi kapolo mnzanga mwa Ambuye:

8 amene ndamtuma kwa inu cifukwa ca ici comwe, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti atonthoze mitima yanu;

9 pamodzi ndi Onesimo, mbale wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ali wa kwa inu. Zonse za kuno adzakuzindikiritsani inu.

10 Aristarko wam'ndende mnzanga akulankhulani inu ndi Marko, msuwani wa Bamaba (amene munalandira zolamulira za kwa iye; akafika kwanu, mumlandire iye),

11 ndi Yesu, wochedwa Yusto, ndiwo a mdulidwe; iwo okha ndiwo anchito anzanga a mu Ufumu wa Mulungu, ndiwo akundikhalira ine conditonthoza mtima.

12 Akulankhulani inu Epafra ndiye wa kwa inu ndiye kapolo wa Yesu Kristu, wakulimbira cifukwa ca inu m'mapemphero ace znasiku onse, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m'cifuniro conse ca Mulungu.

13 Pakuti ndimcitira iye umboni kuti adziwawitsa nayo nchito cifukwa ca inu, ndi iwo a m'Laodikaya, ndi iwo a m'Herapoli.

14 Akulankhulani inu Luka sing'anga wokondedwa, ndi Dema.

15 Lankhulani abalewo a m'Laodikaya, ndi Numfa, ndi Mpingowo wa m'nyumba yao.

16 Ndipo pamene mudamwerenga kalata uyu, amwerengenso mu Mpingo wa ku Laodikaya, ndi inunso muwerenge wa ku Laodikaya,

17 Ndipo nenani kwa Arkipo, Samaliratu utumiki umene udaulandira mwa Ambuye, kuti uukwanitse.

18 Kulankhula ndi dzanja langa, kwa ine Paulo. Kumbukilani zoo mangira zanga, Cisomo cikhale nanu.

Mitu

1 2 3 4