11 amenenso munadulidwa mwa iye ndi mdulidwe wosacitika ndi manja, m'mabvulidwe a thupi, mu mdulidwe wa Kristu;
12 popeza munaikidwa m'manda pamodzi ndi iye muubatizo, momwemonso munaukitsidwa pamodzindi iye m'cikhulupiriro ca macitidwe a Mulungu, amene anamuukitsa iye kwa akufa.
13 Ndipo inu, pokhala akufa m'zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, anakupatsani moyo pamodzi ndi iye, m'mene adatikhululukira ife zolakwa zonse;
14 adatha kutifafanizira ca pa ifeco colembedwa m'zoikikazo, cimene cinali cotsutsana nafe; ndipo anacicotsera pakatipo, ndi kucikhomera ici pamtanda;
15 atabvula maukulu ndi maulamuliro, anawaonetsera poyera, nawagonjetsera nako.
16 Cifukwa cace munthu aliyense asakuweruzeni inu m'cakudya, kapena cakumwa, kapena m'kunena tsiku la phwando, kapena tsiku lokhala mwezi, kapena la Sabata;
17 ndizo mthunzi wa zirinkudzazo; koma thupi ndi la Kristu.