3 amene zolemera zonseza nzeru ndi cidziwitso zibisika mwa iye.
4 Ici ndinena, kuti munthu asakusokeretseni inu ndi mau okopakopa.
5 Pakuti ndingakhale ndiri kwina m'thupi, komatu mumzimu ndiri pamodzi ndi inu, wokondwera pakupenya makonzedwe anu, ndi cilimbiko ca cikhulupiriro canu ca kwa Kristu.
6 Cifukwa cace monga momwe munalandira Kristu Yesu Ambuye, muyende mwa iye,
7 ozika mizu ndi omangirika mwa iye, ndi okhazikika m'cikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kucurukitsa ciiyamiko.
8 Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati cuma, mwa kukonda nzeru kwace, ndi cinyengo copanda pace, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu;
9 pakuti mwa iye cikhalira cidzalo ca Umulungu m'thupi,