16 Mau a Knstu akhalitse mwa inu cicurukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndimayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuyimbira Mulungu ndi cisomo mumtima mwanu.
17 Ndipo ciri conse mukacicita m'mau kapena muncbito, citani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa iye.
18 Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.
19 Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo.
20 Ana inu, mverani akubala inu m'zonse, pakuti ici Ambuye akondwera naco.
21 Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.
22 Akapolo inu, mverani m'zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, wosati ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu ndi mtima wakulinga kumodzi, akuopa Ambuye;