4 kuti ndicionetse ici monga ndiyenera kulankhula.
5 Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kucita macawi nthawi ingatayike.
6 Mau anu akhale m'cisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akarani.
7 Zonse za kwa ine adzakuzindikiritsani Tukiko, mbale wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika ndi kapolo mnzanga mwa Ambuye:
8 amene ndamtuma kwa inu cifukwa ca ici comwe, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti atonthoze mitima yanu;
9 pamodzi ndi Onesimo, mbale wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ali wa kwa inu. Zonse za kuno adzakuzindikiritsani inu.
10 Aristarko wam'ndende mnzanga akulankhulani inu ndi Marko, msuwani wa Bamaba (amene munalandira zolamulira za kwa iye; akafika kwanu, mumlandire iye),