1 MAU a Yehova amene anadza kwa Mika wa ku Morese masiku a Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, amene adaona za Samariya ndi Yerusalemu.
2 Imvani, mitundu ya anthu, inu nonse; tamvera, dziko lapansi, ndi zonse ziri m'mwemo; ndipo Ambuye Yehova akhale mboni yakutsutsa inu, Ambuye m'Kacisi wace wopatulika.
3 Pakuti, taonani, Yehova alikuturuka m'malo mwace, nadzatsika, nadzaponda pa misanje ya dziko lapansi.
4 Ndi mapiri adzasungunuka pansi pa Iye, ndi zigwa zidzang'ambika, ngati sera pamoto, ngati madzi otsanulidwa potsetseremba.
5 Cicitika ici conse cifukwa ca kulakwa kwa Yakobo, ndi macimo a nyumba ya Israyeli. Kulakwa kwa Yakobo nkotani? Si ndiko Samariya? ndi misanje ya Yuda ndi iti? si ndiyo Yerusalemu?
6 Cifukwa cace ndidzaika Samariya ngati mulu wa miyala ya m'munda, ngati zooka m'munda wamphesa; ndipo ndidzataya miyala yace m'cigwa, ndi kufukula maziko ace.