Mika 5 BL92

1 Uzisonkhana tsopano magulu magulu, mwana wamkazi wa magulu iwe; watimangira misasa, adzapanda woweruza wa Israyeli ndi ndodo patsaya.

Aneneratu za kubadwa kwa woweruza m'Israyeli

2 Koma iwe, Betelehemu Efrata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditurukira wina wakudzakhala woweruza m'Israyeli; maturukiro ace ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.

3 Cifukwa cace Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ace adzabwera pamodzi ndi ana a Israyeli,

4 Ndipo adzaimirira, nadzadyetsa nkhosa zace mu mphamvu ya Yehova, m'ukulu wa dzina la Yehova Mulungu wace; ndipo iwo adzakhalabe; pakuti pamenepo Iye adzakhala wamkuru kufikira malekezero a dziko lapansi.

5 Ndipo ameneyo adzakhala Mtendere; pamene a ku Asuri adzalowa m'dziko lathu, ndi pamene adzaponda m'zinyumba zathu, tidzawaukitsira abusa asanu ndi awiri, ndi akalonga asanu ndi atatu.

6 Ndipo iwo adzatha dziko la Asuri ndi lupanga, ndi dziko la Nimrodi, ndilo polowera pace; ndipo adzatilanditsa kwa a ku Asuri pamene alowa m'dziko lathu, pamene aponda m'kati mwa malire athu.

7 Ndipo otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ocokera kwa Yehova, ngati mvula paudzu, yosacedwera munthu, yosalindira ana a anthu.

8 Ndipo, otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama za kuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.

9 Dzanja lako likwezeke pamwamba pa iwo akuyambana nawe, ndi adani ako onse aonongeke.

10 Ndipo kudzacitika tsiku ilo, ati Yehova, ndidzaononga akavalo ako m'kati mwako, ndi kutha magareta ako;

11 ndipo ndidzaononga midzi ya m'dziko lako, ndi kupasula malinga ako onse;

12 ndipo ndidzaononga zanyanga za m'dzanja lako; ndipo sudzakhalanso nao alosi;

13 ndidzaononganso mafano ako osema, ndi zoimiritsa zako pakati pako; ndipo sudzalambiranso nchito za manja ako.

14 Ndipo ndidzazula zifanizo zako m'kati mwako, ndi kutha midzi yako.

15 Ndipo ndidzabwezera amitundu osamvera cilango mu mkwiyo waukali.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7