1 Tamverani tsono conena Yehova: Nyamuka, tsutsana nao mapiri, ndi zitunda zimve mau ako.
2 Tamvani, mapiri inu, citsutsano ca Yehova, ndi inu maziko olimba a dziko lapansi; pakuti Yehova ali naco citsutsano ndi anthu ace, ndipo adzatsutsana ndi Israyeli.
3 Anthu anga inu, ndakucitirani ciani? ndakulemetsani ndi ciani? citani umboni wonditsutsa.
4 Pakuti ndinakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriamu.
5 Anthu anga, kumbukilanitu cofunsira Balaki mfumu ya Moabu, ndi comuyankha Balamu mwana wa Beori, kuyambira ku Sitimu kufikira ku Giligala; kuti mudziwe zolungama za Yehova.
6 Ndidzafika kwa Yehova ndi ciani, ndi kuwerama kwa Mulungu Wam'mwamba? Kodi ndifike kwa Iye ndi nsembe zopsereza, ndi ana a ng'ombe a caka cimodzi?
7 Kodi Yehova adzakondwera nazo nkhosa zamphongo zikwi, kapena ndi mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndipereke mwana wanga woyamba cifukwa ca kulakwa kwanga, cipatso ca thupi langa cifukwa ca kucimwa kwa moyo wanga?
8 Iye anakuuza, munthuwe, comwe ciri cokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti ucite colungama, ndi kukonda cifundo ndi kuyenda modzicepetsa ndi Mulungu wako?
9 Mau a Yehova aitana mudzi, ndi wanzeru aopa dzina lanu; tamverani ndodo, ndi Iye amene anaiika.
10 Kodi m'nyumba ya woipa mukali cuma cosalungama, ndi muyeso wocepa umene ayenera kuipidwa nao?
11 Kodi ndikhoza kuyera ndi miyeso yoipa, ndi thumba la miyala yonyenga?
12 Pakuti anthu ace olemera adzala ndi ciwawa, ndi okhalamo amanena bodza, ndi lilime lao limacita monyenga m'kamwa mwao.
13 Cifukwa cace Inenso ndakukantha ndi kukupweteketsa; ndakupulula cifukwa ca zocimwa zako.
14 Udzadya koma osakhuta; ndi njala yako idzakhala pakati pako; ndipo udzacotsa koma osalanditsa; ndi ici wacilanditsa ndidzacipereka kulupanga.
15 Udzafesa koma osaceka; udzaponda azitona koma osadzola mafuta; udzaponda mphesa koma osamwa vinyo.
16 Pakuti asunga malemba a Omri, ndi nchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda m'uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo cotsonya; ndipo mudzasenza citonzo ca anthu anga.